Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo muchite chikondwerero cholemekeza Chauta masiku asanu ndi aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “ ‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:12
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.


Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;


Napeza munalembedwa m'chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m'misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri,


Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.


ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.


Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.


Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.


Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.


Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.


ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;


Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena;


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa