Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:11 - Buku Lopatulika

11 tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo wopepesera machimo, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:11
10 Mawu Ofanana  

Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yauchimo.


limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;


pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.


amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa