Eksodo 12:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo muzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo muzisunga chikondwerero a Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya. Onani mutuwo |