Eksodo 34:18 - Buku Lopatulika18 Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka m'Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 “Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto. Onani mutuwo |