ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi mu Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.