Masalimo 42:4 - Buku Lopatulika4 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Zinthu izi ndimazikumbukira pamene ndikukhuthula moyo wanga: momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu, kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko pakati pa anthu a pa chikondwerero. Onani mutuwo |
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.