Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 42:5 - Buku Lopatulika

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 42:5
28 Mawu Ofanana  

Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.


Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga; polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wake.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Ndapindika, ndawerama kwakukulu; ndimayenda woliralira tsiku lonse.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa; munthu adzandichitanji?


Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.


Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.


Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.


Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa