Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 42:6 - Buku Lopatulika

6 Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndatayiratu mtima, nchifukwa chake ndikukumbukira Inu Mulungu, pamene ndili ku dziko la Yordani, ku Heremoni ndi ku phiri la Mizara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga kotero ndidzakumbukira Inu kuchokera ku dziko la Yorodani, ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 42:6
14 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.


Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,


Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.


Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa