Zekariya 8:19 - Buku Lopatulika19 Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.” Onani mutuwo |