Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika, ndipo musale zakudya. Musagwire ntchito iliyonse,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “ ‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:7
17 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi chuma chathu chonse.


Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli. Ndinazunza moyo wanga ndi kusala; ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?


Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.


Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza,


podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;


koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa