Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:6 - Buku Lopatulika

6 pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mupereke zonsezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza yopereka mwezi ukakhala, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi nsembe zaufa ndi zopereka za chakumwa, potsata malamulo ake, kuti zitulutse fungo lokoma, nsembe zotentha pa moto, zopereka kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:6
14 Mawu Ofanana  

Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;


Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.


pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.


pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;


Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;


ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;


ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;


ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo, yakutetezera inu;


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;


Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa