Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 2:15 - Buku Lopatulika

15 Ombani lipenga mu Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ombani lipenga m'Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Lizani lipenga mu Ziyoni, lengezani tsiku losala zakudya, itanitsani msonkhano wopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 2:15
8 Mawu Ofanana  

Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.


Ndipo analemba m'makalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;


Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.


Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano.


Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a mu Yerusalemu, ndi anthu onse ochokera m'mizinda ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.


Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.


Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;


Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa