Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 2:16 - Buku Lopatulika

16 sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwawuze kuti adziyeretse; sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Mkwati atuluke mʼchipinda chake, mkwatibwi atuluke mokhala mwake.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 2:16
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.


nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m'malo opatulika.


Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatule; potero Alevi anayang'anira kupha za Paska kwa aliyense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.


wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.


Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.


Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake, likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.


Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.


Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.


nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.


Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sungathe kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.


Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ana aang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.


Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa