Yoweli 2:17 - Buku Lopatulika17 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena aŵanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asaŵaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova, alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova. Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka, kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti, ‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ” Onani mutuwo |