Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 2:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake ndi kuchitira chisoni anthu ake.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 2:18
19 Mawu Ofanana  

Pakuti ku Yerusalemu kudzatuluka otsala, ndi akupulumukawo kuphiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.


Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Pakuti mudzaoneka mu Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'phiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.


Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.


Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.


Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,


Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikulu.


Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu.


Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.


Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo, anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa.


Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.


Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.


Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.


Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa