Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 35:2 - Buku Lopatulika

2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:2
13 Mawu Ofanana  

Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.


Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.


Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.


Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa