Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 35:3 - Buku Lopatulika

3 Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.


Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.


Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse;


Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.


Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.


Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,


Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa