Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 23:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku la chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, lolemekezera Chauta. Pa masiku asanu ndi aŵiri muzidya buledi wosafufumitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 23:6
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.


Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.


Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa