Amosi 8:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pa mutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira, nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu, ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi. Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha. Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake. Onani mutuwo |