Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 2:13
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo.


Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda mu Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Ndipo analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao,


Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska.


Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.


Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa