Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 10:2 - Buku Lopatulika

2 Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Upange malipenga aŵiri asiliva, uchite kusula. Uziimba malipengawo poitana mpingo, ndi pochoka pa mahema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 10:2
14 Mawu Ofanana  

Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;


Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.


Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.


Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.


Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;


Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano.


Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.


Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.


Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.


Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai.


Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa