Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:5 - Buku Lopatulika

5 Koma ananena iwo, pa nthawi ya chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma ananena iwo, pa nthawi la chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:5
17 Mawu Ofanana  

Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.


Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.


Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?


pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.


Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.


Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska.


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.


Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa