Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 146:5 - Buku Lopatulika

5 Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi Mulungu wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 146:5
17 Mawu Ofanana  

Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.


Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.


Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili.


Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.


Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi.


Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa. Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.


Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.


Wolabadira mau adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala.


Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa