Masalimo 146 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 146 1 Tamandani Yehova. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. 2 Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga. 3 Musamadalire mafumu, anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa. 4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi; zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo. 5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi Mulungu wa Yakobo. 6 Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya. 7 Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende, 8 Yehova amatsekula maso anthu osaona, Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi, Yehova amakonda anthu olungama. 9 Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa. 10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse. Tamandani Yehova. |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.