Masalimo 146 - Buku LopatulikaChifooko cha munthu, chikhulupiriko cha Mulungu 1 Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. 2 Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine. 3 Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. 4 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. 5 Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. 6 Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha, 7 ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi. 8 Yehova apenyetsa osaona; Yehova aongoletsa onse owerama; Yehova akonda olungama. 9 Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa. 10 Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi