Masalimo 146:4 - Buku Lopatulika4 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Pamene mpweya wa munthu uchokeratu, munthuyo amabwerera ku dothi, zimene ankafuna kuchita, zimatha tsiku lomwelo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi; zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.