Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 146:9 - Buku Lopatulika

9 Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 146:9
22 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.


Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.


Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.


Yehova agwiriziza ofatsa; atsitsira oipa pansi.


Pa woyera mtima mukhala woyera mtima; pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.


Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.


Yehova adzapasula nyumba ya wonyada; koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake.


Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.


Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;


Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.


Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa