Masalimo 147 - Buku LopatulikaAlemekeze dzina la Mulungu chifukwa cha zokoma amachitira anthu ake 1 Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera. 2 Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele. 3 Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao. 4 Awerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi. 5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha. 6 Yehova agwiriziza ofatsa; atsitsira oipa pansi. 7 Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe; muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze: 8 Amene aphimba thambo ndi mitambo, amene akonzera mvula nthaka, amene aphukitsa msipu pamapiri. 9 Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira. 10 Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu. 11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake. 12 Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. 13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu. 14 Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino. 15 Atumiza lamulo lake kudziko lapansi; mau ake athamanga liwiro. 16 Apatsa chipale chofewa ngati ubweya; awaza chisanu ngati phulusa. 17 Aponya matalala ake ngati zidutsu: Adzaima ndani pa kuzizira kwake? 18 Atumiza mau ake nazisungunula; aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake. 19 Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele. 20 Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi