Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 147:10 - Buku Lopatulika

10 Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mphamvu za kavalo saziyesa kanthu, mphamvu za ankhondo sazisamala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo, kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 147:10
11 Mawu Ofanana  

Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.


Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu? Udzaisiyira ntchito yako kodi?


Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa