Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 147:19 - Buku Lopatulika

19 Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Amadziŵitsa Yakobe mau ake, amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo, malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 147:19
20 Mawu Ofanana  

Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israele machitidwe ake.


Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele.


Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao;


Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.


Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.


Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.


Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.


ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;


Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.


izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;


Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?


Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.


Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.


Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa