Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 147:5 - Buku Lopatulika

5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 147:5
17 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.


Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu; mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu.


Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.


Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.


Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.


Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.


Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake;


Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.


Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa