Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 147:11 - Buku Lopatulika

11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa, amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 147:11
13 Mawu Ofanana  

Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu.


Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.


Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.


Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.


Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.


Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.


Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;


Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;


koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa