Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 126:3 - Buku Lopatulika

3 Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 126:3
19 Mawu Ofanana  

Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.


Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!


Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basani, ndidzawatenganso kozama kwa nyanja,


Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.


Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake.


koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.


Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu.


Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye,


Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake lili loyera.


Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa