Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 33:21 - Buku Lopatulika

21 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:21
11 Mawu Ofanana  

Mudzitamandire ndi dzina lake lopatulika; mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.


Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa chipulumutso chathu; mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.


Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.


Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.


Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.


Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa