Miyambo 3 - Buku LopatulikaMalangizo a kuopa, kukhulupirira, ndi kumvera Yehova 1 Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; 2 pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere. 3 Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; 4 motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu. 5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; 6 umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako. 7 Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa; 8 mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi. 9 Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha; 10 motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. 11 Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; 12 pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Phindu la Nzeru 13 Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; 14 pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. 15 Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. 16 Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. 17 Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. 18 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. 19 Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. 20 Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake; thambo ligwetsa mame. 21 Mwananga, zisachokere kumaso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; 22 ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo. 23 Pompo udzayenda m'njira yako osaopa, osaphunthwa phazi lako. 24 Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa. 25 Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; 26 pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe. Malangizo ena osiyana 27 Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. 28 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu. 29 Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka. 30 Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa. 31 Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. 32 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka. 33 Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. 34 Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. 35 Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi