Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 3:2 - Buku Lopatulika

2 pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 3:2
22 Mawu Ofanana  

Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.


Udzafika kumanda utakalamba, monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yake.


Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.


Inde, udzaona zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israele.


Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.


Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.


Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.


Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m'njira ya chilungamo.


Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.


Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.


Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka, zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.


Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.


Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.


Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;


kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo lili pamwamba padziko.


Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa