Masalimo 1 - Buku LopatulikaKusiyana pakati pa olungama ndi oipa 1 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. 2 Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. 3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo. 4 Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. 5 Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama. 6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi