Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 15:16 - Buku Lopatulika

16 Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:16
13 Mawu Ofanana  

Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.


Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.


Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.


Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.


Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi.


Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.


Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.


Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.


Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa.


Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa