Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 32 - Buku Lopatulika


Mwai wa munthu amene Mulungu wamkhululukira
Salimo la Davide. Chilangizo.

1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.

2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.

3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

5 Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.

6 Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.

7 Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.

9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.

10 Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.

11 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa