Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 32:4 - Buku Lopatulika

4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu lidandipsinja, motero nyonga zanga zidatha, monga amafotera masamba ndi dzuŵa lachilimwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 32:4
15 Mawu Ofanana  

Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu, monga munthu apembedzera mnansi wake!


Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.


Taonani, kuopsa kwanga simudzachita nako mantha; ndi ichi ndikusenzetsani sichidzakulemererani.


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.


Khungu lathu lapserera ngati pamoto chifukwa cha kuwawa kwa njala.


kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.


Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.


Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.


Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa