Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 32:3 - Buku Lopatulika

3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamene ndinali ndisanaulule tchimo langa, thupi langa linali lofooka, chifukwa cha kubuula tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 32:3
26 Mawu Ofanana  

Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.


Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga; ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.


Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine, ndi zowawa zondikungudza sizipuma.


Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?


Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu; ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.


Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.


Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere.


Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.


Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Ana ako aamuna akomoka; agona pamutu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako.


Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake.


Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.


Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.


Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa, nathyola mafupa anga.


Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa