Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 32:1 - Buku Lopatulika

1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 32:1
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.


ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.


Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;


Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.


Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.


Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.


Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.


Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.


Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu; ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse.


Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.


Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa