Afilipi 3:1 - Buku Lopatulika1 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo. Onani mutuwo |
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.