Mtima wanga ukufuna kuti mukachoke kuno, muzipita bwino pa zonse, ndipo mukhale ndi thanzi labwino, monga momwe mukupitira patsogolo mwauzimu. Ndikukhulupirira kuti Mulungu adzakudalitsani pa ulendo wanu.
Mau ambiri ochokera m'Baibulo angatilimbikitse, monga momwe lemba la 3 Yohane 1:2 limatiuza. Mulungu ali ndi malonjezo ambiri kwa ife, ndipo ndikukhulupirira kuti mudzapeza mphamvu ndi chiyembekezo mwa Iye pamene mukupitiriza ulendo wanu.
Zikomo kwambiri chifukwa chobwera, ndipo Mulungu akudalitseni.
Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa. Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake. Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi; ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka. Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza. Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita? Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye? Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye. Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati, Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu, ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa. Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa? Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi? Ndipo anati Yehova, Ndikapeza mu Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo. Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga. Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai. Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga. Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe; komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide padziko lapansi.
ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu.
Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye. Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi. Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.
Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa. Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse, kuti ndiwabwezere. Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka. Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya. Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen. Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika padziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake. Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.
Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.
Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.
Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?
Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira. Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.
Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.
Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.
Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita. Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba. Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife. Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.
Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya, koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi chotengera chilinkutsika, chonga ngati chinsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinai, ndi kutsikira padziko pansi; m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa. Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba. Ndipo chinachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chinatengedwa kunka kumwamba. Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata, ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wotchedwanso Petro, acherezedwako. Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe. ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.
kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake. Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri; popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Chikondi cha pa abale chikhalebe. Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata. Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake. Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo. Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo. Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu. Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino. Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe. Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.
Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.
Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana. Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse. Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea; Moni kwa Apelesi, wovomerezedwayo mwa Khristu. Moni iwo a kwa Aristobulo. Moni kwa Herodiono, mbale wanga. Moni iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye. Moni kwa Trifena, ndi Trifosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye. Moni kwa Rufu, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wake ndi wanga. Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale amene ali nao. Moni kwa Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao. Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsonana kopatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni. Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa. kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;
Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine. nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera, chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha; pakuti mu Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu; ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a achifwamba? Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.
Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.