Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 121:8 - Buku Lopatulika

8 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 121:8
12 Mawu Ofanana  

Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi chuma chathu chonse.


Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.


Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha.


Koma ife tidzalemekeza Yehova kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse. Aleluya.


Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Israele, uyembekezere Yehova, kuyambira tsopano kufikira kosatha.


kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake.


umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.


Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu.


Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa