Masalimo 121 - Buku LopatulikaMulungu Msungi wokhulupirika wa anthu ake Nyimbo yokwerera. 1 Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? 2 Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. 3 Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. 4 Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona. 5 Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. 6 Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku. 7 Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. 8 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi