Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 3:13 - Buku Lopatulika

13 komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 3:13
13 Mawu Ofanana  

Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.


Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?


Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?


ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


Pakuti uchimo, pamene unapeza chifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.


kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;


monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,


Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa.


Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.


koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa