Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:20 - Buku Lopatulika

20 bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyale yofuka sadzayizimitsa, kufikira Iye adzatumiza chiweruziro chikagonjetse.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:20
21 Mawu Ofanana  

Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzampyoza dzanja lake; atero Farao mfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.


Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.


Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.


Pamene Mose adamva ichi chidamkomera pamaso pake.


Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.


Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?


Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,


Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.


Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wogonjetsa kuti akagonjetse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa