Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:42 - Buku Lopatulika

42 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:42
26 Mawu Ofanana  

Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.


Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.


Ena asirira modukidwa tsiku lonse; koma wolungama amapatsa osamana.


Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.


Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.


Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.


Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.


Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake.


Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa