Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:43 - Buku Lopatulika

43 Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:43
17 Mawu Ofanana  

Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse, kuti ndiwabwezere.


Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.


Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.


Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:


Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo;


Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;


Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.


Kumbukirani chochitira inu Amaleke panjira, potuluka inu mu Ejipito;


Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:


Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa